15/09/2026
ACHILIMA ANKANDIKODOLA KUTI NKAWATHANDIZE KOMA MOSACHEDWA KUNATULUKIRA ASILIKALI ACHIZUNGU NDIPO ANATITHAMANGISA PAMALOPO - DUMA
A Ephraim Duma awuza komiti yomwe ikufufuza za ngozi ya ndege yomwe inachitika ku Chikangawa m'chaka cha 2024 kuti anaona ndegeyi itaima mmalele koma pakhomo pa ndege panali wachiwiri wakale wa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima omwe amakodola mokuwa.
Iwo ati zimaoneka kuti A Chilima amafuna atuluke mundegemo koma ati panthawiyo zimaoneka kuti akukokedwa kuti abwelere mkati mwa ndegeyo.
A Duma omwe ati amakhala kwa Senti ku Lilongwe ati panthawi yomwe amaona izi amachoka ku Ekwendeni komwe amagula njinga.
Anamandwa TV